Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 3:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli ankatumikira Yehova moyangʼaniridwa ndi Eli. Masiku amenewo mawu a Yehova sankamveka pafupipafupi. Kuona zinthu mʼmasomphenya sikunkachitikanso kawirikawiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo mwanayo Samuele anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzikamodzi; masomphenya sanaonekeoneke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo mwanayo Samuele anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzikamodzi; masomphenya sanaonekeoneke.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mnyamata uja Samuele ankatumikira Chauta, ndipo Eli ankamuyang'anira. Masiku amenewo mau a Chauta sankamveka kaŵirikaŵiri, ndipo kuwona zinthu m'masomphenya sikunkachitikanso kaŵirikaŵiri.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 3:1
11 Mawu Ofanana  

Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa; palibe aneneri amene atsala ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.


Ngati uthenga wochokera kwa Yehova supezeka anthu amangochita zofuna zawo; koma wodala ndi amene amasunga malamulo.


Ndidzasandutsa anthu kukhala ovuta kupeza kuposa mmene amasowera golide wabwino. Iwo sazidzapezekapezeka kuposa mmene amasowera golide wa ku Ofiri.


Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake, ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake. Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri. Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo, ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.


Tsono Elikana anapita ku mudzi kwawo ku Rama, koma mnyamatayo amatumikira Yehova pansi pa ulamuliro wa wansembe Eli.


Koma Samueli amatumikira pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala.


Pambuyo pake ndidzasankha wansembe wokhulupirika, amene adzachita zimene zili mu mtima ndi mʼmaganizo mwanga. Ndidzakhazikitsa banja lako kolimba ndipo adzatumikira pamaso pa wodzozedwa wanga nthawi zonse.


Ndipo aliyense wotsala wa banja lako adzabwera ndi kugwada pamaso pake kupempha ndalama kapena chakudya.’ Adzati, ‘Chonde ndiloleni kuti ndizithandizako pa ntchito iliyonse ya unsembe kuti ndipeze chakudya.’ ”


Samueli anagona mpaka mmawa. Atadzuka anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova. Iye anachita mantha kumuwuza Eli za masomphenya ake.


Yehova anapitiriza kuoneka ku Silo, ndipo kumeneko anadziwulula yekha kwa Samueli mwa mawu ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa