Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 26:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Sauli anamanga msasa wake mʼmbali mwa njira yopita ku phiri la Hakila moyangʼanana ndi Yesimoni. Koma Davide anali mʼchipululumo. Davide ataona kuti Sauli amamulondola mpaka kumeneko,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Saulo namanga zithando m'phiri la Hakila kupenya kuchipululu kunjira. Koma Davide anakhala kuchipululu, naona kuti Saulo alikumfuna kuchipululu komweko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Saulo namanga zithando m'phiri la Hakila kupenya kuchipululu kunjira. Koma Davide anakhala kuchipululu, naona kuti Saulo alikumfuna kuchipululu komweko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Adamanga zithando zankhondo pa phiri la Hakila, limene lili pambali pa mseu, chakuvuma kwa Yesimoni. Koma Davide adakhalabe kuchipululuko. Tsono ataona kuti Saulo akumlondola,

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 26:3
6 Mawu Ofanana  

Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, moona mtima ine ndimakufunafunani; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka inu, mʼdziko lowuma ndi lotopetsa kumene kulibe madzi.


Davide anaona kuti Sauli akufunafuna kuti amuphe. Nthawiyi nʼkuti Davide ali mʼchipululu cha Zifi ku Horesi.


Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya ndipo anamuwuza kuti, “Davide akubisala kwathu, mʼmapanga a ku Horesi, mʼphiri la Hakila, kummwera kwa Yesimoni.


Iye anafika ku makola a nkhosa amene anali mʼmbali mwa njira. Kumeneko kunali phanga, ndipo Sauli analowa mʼphangamo kuti akadzithandize. Davide ndi anthu ake ankabisala mʼkati mwenimweni mwa phangalo.


Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya nati, “Davide akubisala ku phiri la Hakila, limene limayangʼanana ndi Yesimoni.”


iye anatumiza anthu okazonda ndipo anapeza kuti Sauli wafikadi ndithu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa