Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 2:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Yehova asaukitsa, nalemeretsa; achepetsa, nakuzanso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Yehova asaukitsa, nalemeza; achepetsa, nakuzanso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Chauta amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:7
17 Mawu Ofanana  

Yehu anayimirira nakalowa mʼnyumba. Pamenepo mneneriyo anakhuthulira mafuta pamutu pa Yehu ndipo ananena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndikukudzoza kukhala mfumu ya Israeli, anthu a Yehova.


Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu; Inu ndinu wolamulira zinthu zonse. Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu, kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse.


Hezekiya anali ndi chuma ndi ulemu wambiri ndipo anamanga nyumba zosungiramo chuma cha siliva wake ndi golide ndi za miyala yokongola, zokometsera zakudya, zishango ndi mtundu uliwonse wa zinthu zamtengowapatali.


Iyeyo anamanga midzi ndipo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, pakuti Mulungu anamupatsa chuma chambiri.


nati, “Ndinatuluka maliseche mʼmimba mwa amayi anga, namonso mʼmanda ndidzalowa wamaliseche. Yehova ndiye anapereka ndipo Yehova watenga; litamandike dzina la Yehova.”


Uyangʼane aliyense wodzikweza ndipo umutsitse, uwapondereze oyipa onse pamalo pomwe alilipo.


Iye amakweza anthu wamba, ndipo iwo amene akulira amawayika pa malo otetezedwa.


chifukwa cha ukali wanu waukulu, popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali.


Koma ndi Mulungu amene amaweruza: Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.


Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse.


Wolemera ndi wosauka ndi ofanana; onsewa anawalenga ndi Yehova.


Yehova Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku limene adzatsitse onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu,


“Ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina. Mudzakhala anthu onyozeka pakati pa anthu.


Mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine ndine Yehova amene ndimafupikitsa mitengo yayitali ndi kutalikitsa mitengo yayifupi. Ndimawumitsa mitengo yabiriwiri ndi kubiriwitsa mitengo yowuma. “ ‘Ine Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichita.’ ”


Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa