Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 2:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Amene kale anali okhuta tsopano akukagula chakudya, koma iwo amene anali ndi njala sakumvanso njala. Amene anali wosabereka, wabereka ana aamuna asanu ndi awiri, koma iye wobereka ana ambiri watsala yekha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Amene anakhuta anakasuma chakudya; koma anjalawo anachira; inde chumba chabala asanu ndi awiri; ndipo iye amene ali ndi ana ambiri achita liwondewonde.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Amene anakhuta anakasuma chakudya; koma anjalawo anachira; inde chumba chabala asanu ndi awiri; ndipo iye amene ali ndi ana ambiri achita liwondewonde.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Anthu amene kale adaali okhuta, tsopano akusuma, koma amene kale adaali ndi njala, tsopano akukhuta. Chumba chabala ana asanu ndi aŵiri, koma wobereka ana ambiri watsala yekha.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:5
11 Mawu Ofanana  

Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake monga mayi wa ana wosangalala. Tamandani Yehova.


Mikango itha kulefuka ndi kumva njala koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.


Dziko likulira ndipo likunka likutha. Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota. Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala. Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.


“Sangalala, iwe mayi wosabala, iwe amene sunabalepo mwana; imba nyimbo, ndi kufuwula mwachimwemwe, iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka; chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri kuposa mkazi wokwatiwa,” akutero Yehova.


Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomoka ndipo akupuma wefuwefu. Dzuwa lake lalowa ukanali usana; anamuchititsa manyazi ndipo wathedwa nzeru. Otsala ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo kuti awaphe ndi lupanga,” akutero Yehova.


Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino koma anachotsa olemera wopanda kanthu.


“Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo.


Pakuti kwalembedwa kuti, “Sangalala, iwe mayi wosabala, amene sunabalepo mwana; imba nthungululu ndi kufuwula mwachimwemwe, iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka; chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri kuposa mkazi wokwatiwa.”


Mwanayo adzakupatseni moyo watsopano ndi kukuthandizani pa ukalamba wanu. Inde, mpongozi wanu amene amakukondani, amenenso waonetsa kuti ali wopambana kwa inu kuposa ana aamuna asanu ndi awiri, ndiye wakubalirani mwanayu.”


Motero Hana anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Samueli, popeza anati, “Ndinachita kumupempha kwa Yehova.”


Tsono popeza Yehova sanamupatse Hana ana, mkazi mnzakeyo ankamuyamba dala ndi cholinga chomukwiyitsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa