Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 2:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Mauta a anthu ankhondo athyoka koma anthu ofowoka avala dzilimbe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Mauta a amphamvu anathyoka, koma okhumudwawo amangiridwa ndi mphamvu m'chuuno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mauta a amphamvu anathyoka, koma okhumudwawo amangiridwa ndi mphamvu m'chuuno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ankhondo amphamvu mauta ao athyoka, koma anthu ofooka avala dzilimbe.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:4
16 Mawu Ofanana  

Inu munandiveka ndi mphamvu yokachitira nkhondo, munachititsa kuti ndigonjetse adani anga.


Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe, ndipo mauta awo anathyoka.


pakuti mphamvu ya oyipa idzasweka, koma Yehova amasunga olungama.


Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu; ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu; ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”


Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo; amatentha zishango ndi moto.


Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka, zishango ndi malupanga, zida zankhondo. Sela


Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa kapena kufa pamodzi ndi ophedwa. Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.


Iye amalimbitsa ofowoka ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.


Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene likukuthirani nkhondo ndipo mʼmatenti mwawo ndikutsala anthu ovulala okhaokha, amenewo adzabwera ndi kudzatentha mzinda uno.”


Pakuti wowononga wafika kudzamenyana ndi Babuloni, ankhondo ake agwidwa, ndipo mauta awo athyoka. Paja Yehova ndi Mulungu wobwezera chilango; adzabwezera kwathunthu.


Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.


Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa.


Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.


Kodi ndinenenso chiyani? Nthawi yandichepera yoti ndinene za Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita, Davide, Samueli ndi aneneri,


anazimitsa moto waukali, ndipo anapulumuka osaphedwa ndi lupanga. Anali ofowoka koma analandira mphamvu; anasanduka amphamvu pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani awo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa