Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 2:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndipo Hana anapemphera nati, “Moyo wanga ukukondwera mwa Yehova; Ndiyenda mwa tukumutukumu chifukwa cha Yehova. Pakamwa panga pakula ndi kuseka adani anga mowanyogodola. Ndikukondwa chifukwa mwandipulumutsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Hana adapemphera nati, “Mtima wanga ukukondwa chifukwa cha zimene Chauta wandichitira, Ndikuyenda ndi mdidi chifukwa cha Chauta. Pakamwa panga pakula nkuseka adani anga monyodola. Ndakondwa kwambiri chifukwa mwandipulumutsa.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:1
37 Mawu Ofanana  

Tsono motsogozedwa ndi Yehosafati, anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anabwerera ku Yerusalemu mokondwera pakuti Yehova anawagonjetsera adani awo.


Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu ndiye anali wotsogolera pa mapemphero achiyamiko. Panalinso Bakibukiya amene anali wachiwiri pakati pa abale ake. Kuwonjezera apo panalinso Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.


“Ndasokerera chiguduli pa thupi langa ndipo ndayika mphamvu zanga pa fumbi.


Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; Iye wakhala chipulumutso changa.


Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika; mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.


Iye wakwezera nyanga anthu ake, matamando a anthu ake onse oyera mtima, Aisraeli, anthu a pamtima pake. Tamandani Yehova.


Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo. Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.


Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu, Yehova ayankhe zopempha zako zonse.


Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake. Sela


Pamenepo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova ndi kusangalala ndi chipulumutso chake.


Inu Ambuye tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalengeza matamando anu.


Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu, kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.


Ndidzadula nyanga za onse oyipa koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.


Pakuti Inu ndiye ulemerero wawo ndi mphamvu yawo ndipo mwa kukoma mtima kwanu Inu mumakweza nyanga yathu.


Ndithudi, chishango chathu ndi cha Yehova, Mfumu yathu kwa Woyerayo wa Israeli.


Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye, ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.


kuti ndilengeze za matamando anu pa zipata za ana aakazi a Ziyoni, kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.


Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati; mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga.


Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi: “Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wakwezeka mʼchigonjetso. Kavalo ndi wokwera wake, Iye wawaponya mʼnyanja.


Miriamu anawayimbira nyimbo iyi: “Imbirani Yehova, chifukwa iye wapambana. Kavalo ndi wokwerapo wake Iye wawamiza mʼnyanja.”


Pemphero la mneneri Habakuku potsata mayimbidwe a Sigionoti.


komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.


Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife mu nyumba ya mtumiki wake Davide.


Sikuti izi zili chomwechi chabe, koma timakondweranso mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Kudzera mwa Iye, ife tsopano tayanjanitsidwa ndi Mulungu.


Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa; nyanga zake zili ngati za njati. Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina, ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi. Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu; nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.”


Pakuti ochita mdulidwe weniweni ndife. Ife amene timatumikira Mulungu motsogozedwa ndi Mzimu. Ife amene timanyadira Khristu, ndipo sitidalira zinthu za thupi


Nthawi zonse muzikondwa mwa Ambuye. Ndikubwerezanso; muzikondwa!


Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.


Ngakhale kuti simunamuone, mumamukonda; ndipo ngakhale kuti simukumuona tsopano, mumamukhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka.


“Kondwerani chifukwa cha iye inu kumwamba! Kondwerani oyera mtima ndi atumwi ndi aneneri! Mulungu wamuweruza iye monga momwe anakuchitirani inu.”


Tsono popeza Yehova sanamupatse Hana ana, mkazi mnzakeyo ankamuyamba dala ndi cholinga chomukwiyitsa.


Izi zimachitika chaka ndi chaka. Hana ankati akamapita ku Nyumba ya Yehova mkazi mnzakeyo ankamunyogodola. Choncho Hana ankangokhalira kulira osafuna ndi kudya komwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa