Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 15:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsopano pita kathire nkhondo Aamaleki ndi kuwononga kwathunthu zinthu zonse zimene ali nazo. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe. Mukaphe amuna ndi akazi, ana ndi makanda, ngʼombe ndi nkhosa, ngamira ndi abulu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pitani tsono, mukaŵathire nkhondo Aamalekewo, mukaononge kwathunthu zinthu zao zonse. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe, mukaphe amuna, akazi, ana ndi makanda omwe. Mukaphenso ng'ombe, nkhosa, ngamira ndi abulu onse.’ ”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 15:3
20 Mawu Ofanana  

Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau.


Iye anandifunsa, “Iwe ndiwe yani?” Ine ndinayankha kuti, “Ndine Mwamaleki.”


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba izi mʼbuku kuti zidzakumbukirike ndipo uwonetsetse kuti Yoswa amve zimenezi, chifukwa Ine ndidzafafaniziratu Amaleki pa dziko lapansi, kotero kuti palibe amene adzawakumbukire.”


Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane.


Kenaka Balaamu anaona Aamaleki ndipo ananena uthenga wake uwu: “Aamaleki anali oyamba mwa mitundu ya anthu koma potsiriza pake adzawonongeka.”


Tsopano iphani munthu wamwamuna aliyense. Ndiponso iphani mayi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna,


Iwo analanda mzindawo ndi midzi ndi kupha mfumu yake pamodzi ndi onse okhala mʼmenemo. Anachita ndi mzinda wa Debri pamodzi ndi mfumu yake zofanana ndi zimene anachita ndi mzinda wa Libina ndi wa Hebroni.


Anachita nkhondo mwamphamvu ndi kugonjetsa Aamaleki. Choncho anapulumutsa Aisraeli mʼmanja mwa anthu amene ankawalanda zinthu zawo.


Ndipo Yehova anakutumani kuti, ‘Pitani mukawononge kwathunthu Aamaleki, anthu oyipa aja. Mukachite nawo nkhondo mpaka kuwatheratu.’


Koma Sauli ndi ankhondo ake sanaphe Agagi, sanaphenso nkhosa ndi ngʼombe zabwino ngakhalenso ana angʼombe ndi ana ankhosa onenepa. Chilichonse chimene chinali chabwino sanachiphe. Koma zonse zimene zinali zoyipa ndi zachabechabe anaziwononga.


Kunena za Nobi, mzinda wa ansembe, Sauli anapha amuna ndi amayi, ana ndi makanda pamodzi ndi ngʼombe, abulu ndi nkhosa.


Davide ankati akathira nkhondo dera lina, sankasiya munthu wamoyo, mwamuna kapena mkazi, koma ankatenga nkhosa, ngʼombe, abulu, ngamira ndi zovala, pambuyo pake nʼkubwerera kwa Akisi.


Tsono Davide anawakantha kuyambira madzulo atsikulo mpaka madzulo a tsiku linalo. Palibe anapulumuka kupatula anyamata 400 amene anakwera pa ngamira nʼkuthawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa