Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 11:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Tsono Sauli anawuza amithenga ochokera ku Yabesi aja kuti, “Mukawawuze anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti mawa nthawi ya masana adzapulumutsidwa.” Pamene amithengawo anapita ndi kukafotokoza nkhani imeneyi kwa anthu a ku Yabesi, iwo anasangalala kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona chipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabesi; nakondwera iwowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona chipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabesi; nakondwera iwowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndipo adauza amithenga a ku Yabesi aja kuti, “Mukaŵauze anthu akwanu kuti maŵa, dzuŵa likuwomba mtengo, adzapulumutsidwa.” Anthu a ku Yabesi atamva uthengawu, adasangalala zedi.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 11:9
7 Mawu Ofanana  

iye anatuma amithenga kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti akayankhule nawo kuti, “Yehova akudalitseni poonetsa kukoma mtima kwanu kwa Sauli mbuye wanu pomuyika mʼmanda.


anthu awo onse olimba mtima anapita kukatenga mitembo ya Sauli ndi ana ake ndipo anabwera nayo ku Yabesi. Anakwirira mafupa awo pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri.


Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, adani anga, amene anali amphamvu kuposa ine.


Kenaka anafunsa kuti, ‘Kodi mu fuko la Israeli ndani amene sanabwere pamaso pa Yehova ku Mizipa?’ ” Tsono panapezeka kuti panalibe ndi mmodzi yemwe wochokera ku Yabesi Giliyadi amene anapita ku msonkhano ku misasa kuja.


Choncho anthu a ku Yabesi anawuza Nahasi kuti, “Mawa tidzadzipereka kwa inu ndipo inu mudzachite nafe chilichonse chokukomerani.”


Pamenepo Sauli anawasonkhanitsa ku Bezeki nawawerenga, ndipo Aisraeli analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000.


Pamene anthu a ku Yabesi Giliyadi anamva zimene Afilisti anachitira Sauli,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa