Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 11:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Koma Nahasi Mwamoni uja anayankha kuti, “Ndidzachita nanu pangano pokhapokha nditakolowola diso lakumanja la aliyense wa inu kuti ndichititse manyazi Aisraeli onse.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ndipo Nahasi Mwamoni ananena nao, Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso a ku dzanja lamanja anu onse akolowoledwe; potero ndidzanyazitsa Aisraele onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Nahasi Mwamoni ananena nao, Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso a ku dzanja lamanja anu onse akolowoledwe; potero ndidzanyazitsa Aisraele onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Koma Nahasi adaŵauza kuti, “Ndidzachita nanu chipangano pokhapokha aliyense nditamkolowola diso la ku dzanja lamanja, kuti pakutero ndichititse manyazi Aisraele onse.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 11:2
11 Mawu Ofanana  

Iwo anati, “Sitingachite zimenezo, kupereka mlongo wathu kwa munthu wosachita mdulidwe. Chimenecho ndi chinthu cha manyazi kwa ife.


“ ‘Musamumvere Hezekiya. Zimene mfumu ya ku Asiriya ikunena ndi izi: Pangani mtendere ndi ine ndipo mutuluke mu mzinda. Mukatero aliyense wa inu adzadya mphesa ndi nkhuyu za mʼmunda mwake ndiponso adzamwa madzi a mʼchitsime chake,


Mwachititsa kuti tikhale chochititsa manyazi kwa anthu a mitundu ina, chonyozeka ndi chothetsa nzeru kwa iwo amene atizungulira.


Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.” Atamva zimenezi, Mose anaphimba nkhope yake chifukwa anaopa kuona Mulungu.


Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziweto zake, koma chifundo cha munthu woyipa ndi chakhanza.


Kenaka inakolowola maso a Zedekiya ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni.


Kuwonjezera apo, sunatilowetse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kapena kutipatsa malo wolima ndi minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuchotsa maso a anthuwa? Ayi, sitibwera!”


Afilisti anamugwira ndipo anamukolowola maso. Kenaka anapita naye ku Gaza atamumanga ndi maunyolo achitsulo. Kumeneko anakhala wa pamphero mu ndende.


Choncho anthu a ku Yabesi anawuza Nahasi kuti, “Mawa tidzadzipereka kwa inu ndipo inu mudzachite nafe chilichonse chokukomerani.”


“Koma mutaona kuti Nahasi mfumu ya Amoni inkabwera kudzamenyana nanu, inu munandiwuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu kuti itilamulire,’ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye anali mfumu yanu.


Davide anafunsa anthu amene anayima pafupi naye kuti, “Kodi adzamuchita chiyani munthu amene adzapha Mfilisiti uyu ndi kuchotsa chitonzo pakati pa Israeli? Mfilisiti wosachita mdulidweyu ndi ndani kuti azinyoza gulu lankhondo la Mulungu wamoyo?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa