1 Samueli 10:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 “Ndipo udzapyola pamenepo ndi kufika ku mtengo wa thundu wa ku Tabori. Kumeneko udzakumana ndi anthu atatu akupita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Mulungu ku Beteli. Mmodzi adzakhala atanyamula ana ambuzi atatu, wina atanyamula malofu atatu a buledi, ndi winayo atanyamula thumba la vinyo. Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Betele, wina wonyamula anaambuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Betele, wina wonyamula anaambuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Tsono utabzola pamenepo, ufika pa mtengo wogudira wa ku Tabori. Kumeneko ukumana ndi anthu atatu, wina atanyamula anaambuzi atatu, wina atanyamula mitanda itatu ya buledi, ndipo wina atanyamula thumba lachikopa la vinyo, akupita kukapereka nsembe kwa Mulungu ku Betele. Onani mutuwo |