1 Samueli 10:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Sauli anati, “Iye anatitsimikizira kuti abulu anapezeka.” Koma sanawawuze amalume akewo za nkhani ija ya ufumu imene Samueli anamuwuza. Onani mutuwoBuku Lopatulika16 Ndipo Saulo anati kwa mbale wa atate wake, Anatiuza momveka kuti abuluwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitse mau aja Samuele ananena za ufumuwo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo Saulo anati kwa mbale wa atate wake, Anatiuza momveka kuti abuluwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitse mau aja Samuele ananena za ufumuwo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Saulo adati, “Samuele adatiwuza bwino lomwe kuti abuluwo adapezeka.” Koma sadanene kanthu za nkhani ya ufumu ija imene Samuele adaamuuza. Onani mutuwo |