Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 1:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Tsono popeza Yehova sanamupatse Hana ana, mkazi mnzakeyo ankamuyamba dala ndi cholinga chomukwiyitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukulu, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukulu, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono chifukwa choti Chauta sadampatse ana, mkazi mnzake uja ankangomnyodola ndi kumpeputsa, kuti amkwiyitse.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 1:6
8 Mawu Ofanana  

Rakele ataona kuti sakumuberekera Yakobo ana, anayamba kumuchitira nsanje mʼbale wake. Choncho anati kwa Yakobo, “Undipatse ana kapena apo ayi ndingofa!”


Ndipo Mikala mwana wa Sauli sanakhalenso ndi mwana mpaka anamwalira.


Amachitira nkhanza mayi wosabala ndi mayi amene alibe mwana, ndipo sakomera mtima mkazi wamasiye.


“Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka, ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.


“ ‘Usakwatire mchemwali wa mkazi wako ndi kumagonana naye mkazi wakoyo ali moyo ngati wopikisana naye.


Anatinso kwa abambo ake, “Ndikupempheni chinthu ichi: Mundilole ndikayendeyende ku mapiri miyezi iwiri ndizikalira pamodzi ndi anzanga chifukwa ndikufa ndikanali namwali wosadziwa mwamuna.”


Izi zimachitika chaka ndi chaka. Hana ankati akamapita ku Nyumba ya Yehova mkazi mnzakeyo ankamunyogodola. Choncho Hana ankangokhalira kulira osafuna ndi kudya komwe.


Ndipo Hana anapemphera nati, “Moyo wanga ukukondwera mwa Yehova; Ndiyenda mwa tukumutukumu chifukwa cha Yehova. Pakamwa panga pakula ndi kuseka adani anga mowanyogodola. Ndikukondwa chifukwa mwandipulumutsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa