Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 1:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Chaka ndi chaka Elikana ankachoka ku mudzi kwawo kupita ku Silo kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Yehova Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi amene anali ansembe a Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m'mzinda mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Yehova wa makamu mu Silo. Ndipo pomwepo panali ana aamuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m'mudzi mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Mulungu wa makamu m'Silo. Ndipo pomwepo panali ana amuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Chaka ndi chaka Elikana ankapita ku Silo kuchokera ku mzinda kwao, kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Chauta Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana aŵiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, amene anali ansembe a Chauta.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 1:3
22 Mawu Ofanana  

Anasiya nyumba ya ku Silo, tenti imene Iyeyo anayimanga pakati pa anthu.


“Muzichita zikondwerero zolemekeza Ine katatu pa chaka.


“Amuna onse azionekera pamaso pa Ambuye Yehova katatu pa chaka.


Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu wa Israeli, katatu pa chaka.


Chaka chilichonse makolo ake ankapita ku Yerusalemu ku phwando la Paska.


Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu katatu pa chaka ku malo amene Iye adzasankha. Pa Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti, pa Chikondwerero cha Masabata ndi pa Chikondwerero cha Misasa. Munthu aliyense asadzapite pamaso pa Yehova wopanda kanthu mʼmanja mwake.


Atagonjetsa dziko lonse Aisraeli anasonkhana ku Silo ndipo anayimikako tenti ya msonkhano.


Choncho anthu a fuko la Dani ankapembedza fano limene Mika anapanga nthawi yonse pamene nyumba ya Mulungu inali ku Silo.


Ndipo anati, ‘Paja ku Silo kuli chikondwerero cha chaka ndi chaka cholemekeza Yehova. Tsono Silo ali kumpoto kwa Beteli, kummawa kwa msewu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu, ndiponso kummwera kwa Lebona.’ ”


Elikana ndi banja lake lonse anapita kukapereka nsembe ya pa chaka kwa Yehova ndi kukakwaniritsa malonjezo ake.


Tsiku lina atatha kudya ndi kumwa ku Silo kuja, Hana anayimirira kukapemphera. Nthawiyi nʼkuti wansembe Eli atakhala pa mpando pa khomo la Nyumba ya Yehova.


Pakati pawo panalinso Ahiya amene ankavala efodi. Iye anali mwana wa Ahitubi, mʼbale wake wa Ikabodi mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo. Koma palibe amene anadziwa kuti Yonatani wachoka.


Chaka chilichonse amayi ake ankamusokera kamkanjo ndi kukamupatsa akamapita ndi mwamuna wake kukapereka nsembe za pa chaka.


“ ‘Ndipo chimene chidzachitike kwa ana ako awiriwa, Hofini ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwe. Onse awiri adzafa pa tsiku limodzi.


Pakuti ndinamudziwitsa kuti Ine ndikhoza kulanga banja lake kwamuyaya chifukwa cha zoyipa zimene ana ake ankadziyipitsa nazo. Iye ankadziwa zimenezi koma osawaletsa.


Ndipo Bokosi la Chipangano la Yehova linalandidwa, ndiponso ana awiri Eli, Hofini ndi Finehasi anaphedwa.


Choncho anatuma anthu ku Silo ndipo anakatenga Bokosi la Chipangano cha Yehova Wamphamvuzonse amene amakhala pa akerubi. Ndipo ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi anatsagana nalo Bokosi la Chipangano cha Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa