Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 8:17 - Buku Lopatulika

17 ndipo musalingirira choipa m'mtima mwanu yense pa mnzake; nimusakonde lumbiro lonama; pakuti izi zonse ndidana nazo, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 ndipo musalingirira choipa m'mtima mwanu yense pa mnzake; nimusakonde lumbiro lonama; pakuti izi zonse ndidana nazo, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Musamachitirane chiwembu, musamakonde kulumbira zonama, pakuti zonsezi ndimadana nazo.” Ndikutero Ine Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 musamachitire mnzanu chiwembu, musamakonde kulumbira zonama. Zonsezi Ine ndimadana nazo,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 8:17
19 Mawu Ofanana  

Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.


Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.


Usapangire mnzako chiwembu; popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.


zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu.


Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.


Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?


Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.


Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho.


Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa, osakhoza kupenyerera chovuta, mupenyereranji iwo akuchita mochenjerera, ndi kukhala chete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini;


musazunza mkazi wamasiye, kapena ana amasiye, mlendo kapena waumphawi; ndipo nnena mmodzi wa inu alingirire m'mtima mwake kumchitira choipa munthu mnzake.


Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,


Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.


Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'chuma chake choipa.


Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa