Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 14:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lao lina kunka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kunka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lao lina kunka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kunka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsiku limenelo madzi a moyo adzatuluka ku Yerusalemu. Theka la madziwo lidzathira m'nyanja yakuvuma, theka lina lidzathira m'nyanja yakuzambwe. Zimenezi zidzachitika pa nthaŵi yachilimwe ndi yachisanu yomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Tsiku limenelo madzi amoyo adzatuluka mu Yerusalemu, theka lidzapita ku nyanja ya kummawa ndipo theka lina ku nyanja ya kumadzulo, nthawi yachilimwe ndi nthawi yozizira yomwe.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 14:8
18 Mawu Ofanana  

Ndiwe kasupe wa m'minda, chitsime cha madzi amoyo, ndi mitsinje yoyenda yochokera ku Lebanoni.


Ndipo mchenga wong'azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m'malo a ankhandwe m'mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.


Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.


ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.


koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu.


Ndipo kudzachitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m'mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi akasupe adzatuluka m'nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi chigwa cha Sitimu.


Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m'mabande ake; pakuti ku Ziyoni kudzatuluka chilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova.


Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo paphiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera.


ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.


Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.


koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.


Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake.


Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa