Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 14:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo banja la ku Ejipito likapanda kukwera, losafika, sudzawagwera kodi mliri umene Yehova adzakantha nao amitundu osakwera kusunga chikondwerero cha Misasa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo banja la ku Ejipito likapanda kukwera, losafika, sudzawagwera kodi mliri umene Yehova adzakantha nao amitundu osakwera kusunga chikondwerero cha Misasa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ngati anthu a ku Ejipito sadzapita kukaonekera kumeneko, adzalandiranso chilango chonga chomwe Chauta adzalange nacho mtundu wina uliwonse wa anthu osapita kukachita chikondwerero chamisasa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ndipo ngati anthu a ku Igupto sadzapita ndi kukakhala nawo kumeneko, adzakhala wopanda mvula. Yehova adzabweretsa pa iwo mliri umene analangira mitundu ina ya anthu imene sinapite ku Chikondwerero cha Misasa.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 14:18
8 Mawu Ofanana  

Pakuti mtundu ndi ufumu umene udzakana kukutumikira udzaonongeka; inde mitundu imeneyo idzasakazidwa ndithu.


Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzake, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira kulinzake, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova.


Nena ndi ana a Israele, kuti, Tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uno wachisanu ndi chiwiri pali chikondwerero cha Misasa ya Yehova, masiku asanu ndi awiri.


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.


Ndipo mliri umene Yehova adzakantha nao mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: nyama yao idzaonda akali chilili pa mapazi ao, ndi maso ao adzapuwala m'funkha mwao, ndi lilime lao lidzanyala m'kamwa mwao.


Momwemonso mliri wa pa akavalo, nyuru, ngamira, ndi abulu, ndi nyama zonse zokhala m'misasa iyo, udzakhala ngati mliri uwo.


Ili ndi tchimo la Ejipito, ndi tchimo la amitundu onse osakwerako kusunga chikondwerero cha Misasa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa