Zekariya 12:6 - Buku Lopatulika6 Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwake, mu Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwake, m'Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsiku limenelo mafuko a ku Yuda ndidzaŵasandutsa ngati mbaula yotentha pakati pa nkhuni, ngati nsakali yoyaka pakati pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yoŵazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma anthu a ku Yerusalemu adzakhalabe mwamtendere mumzinda mwao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 “Pa tsiku limenelo ndidzasandutsa atsogoleri a Yuda kukhala ngati mbawula yotentha pakati pa nkhuni, ngati sakali yoyaka pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yowazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma Yerusalemu sadzasuntha pa malo ake. Onani mutuwo |