Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 12:11 - Buku Lopatulika

11 Tsiku lomwelo kudzakhala maliro aakulu mu Yerusalemu, ngati maliro a Hadadirimoni m'chigwa cha Megido.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Tsiku lomwelo kudzakhala maliro akulu m'Yerusalemu, ngati maliro a Hadadirimoni m'chigwa cha Megido.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsiku limenelo kulira maliro ku Yerusalemu kudzakula monga m'mene kunaliri polira Hadadirimoni m'chigwa cha ku Megido.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Pa tsiku limenelo mudzakhala kulira kwakukulu mu Yerusalemu, monga kulira kwa ku Hadadi-Rimoni ku chigwa cha Megido.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 12:11
7 Mawu Ofanana  

Masiku ake Farao Neko mfumu ya Aejipito anakwerera mfumu ya Asiriya ku mtsinje wa Yufurate; ndipo mfumu Yosiya anatuluka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.


Koma Yosiya sanatembenuke nkhope yake kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ochokera m'kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m'chigwa cha Megido.


Pamenepo anyamata ake anamtulutsa m'galeta, namuika m'galeta wachiwiri anali naye, nabwerera naye ku Yerusalemu; nafa iye naikidwa m'manda a makolo ake. Ayuda onse ndi Yerusalemu nalira Yosiya.


Ndipo dziko lidzalira, banja lililonse pa lokha; banja la nyumba ya Davide pa lokha, ndi akazi ao pa okha; banja la nyumba ya Natani pa lokha, ndi akazi ao pa okha;


ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.


Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu. Amen.


Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa mu Chihebri Armagedoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa