Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 11:17 - Buku Lopatulika

17 Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga padzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga pa dzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 “Tsoka kwa mbusa wanga wopandapakeyo, amene amasiya nkhosa! Amkanthe ndi lupanga pa mkono, ndi pa diso lake lakumanja. Mkono wakewo ufwape, ndipo diso lakelo lichite khungu kotheratu!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 “Tsoka kwa mʼbusa wopandapake, amene amasiya nkhosa! Lupanga limukanthe pa mkono wake ndi pa diso lake lakumanja! Mkono wake ufote kotheratu, diso lake lamanja lisaonenso.”

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 11:17
28 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe mu Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso.


Pakuti Yehova watsanulira pa inu mzimu wa tulo togonetsa, natseka maso anu, ndiwo aneneri; naphimba mitu yanu, ndiwo alauli.


Ndani wapanga mulungu, kapena kusungunula fano losema losapindula kanthu?


Nkhalamba ndi wolemekezeka ndiye mutu, ndi mneneri wophunzitsa zonama ndiye mchira.


Yehova atero: Tsikira kunyumba ya mfumu ya Yuda, ndi kunena komweko mau awa,


Tsoka abusa amene athetsa nabalalitsa nkhosa za busa langa! Ati Yehova.


Taonani, Ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zao, ndi matukutuku ao achabe; koma Ine sindinatume iwo, sindinauze iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova.


Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu waowao, chinkana sanaone kanthu.


Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?


Pakuti aterafi anena zopanda pake, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto achabe, asangalatsa nazo zopanda pake; chifukwa chake ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Dzitengerenso zipangizo za mbusa wopusa.


Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula Kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golide wa Kachisi, wadzimangirira.


Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao; kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo ndingawachiritse.


Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona.


Ndipo chiyani tsono? Ichi chimene Israele afunafuna sanachipeze; koma osankhidwawo anachipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima;


Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu padziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.


Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m'banja lako musakhalenso nkhalamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa