Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 11:14 - Buku Lopatulika

14 Pamenepo ndinadula ndodo yanga ina, ndiyo Chomanganitsa, kuti ndithetse chibale cha pakati pa Yuda ndi Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pamenepo ndinadula ndodo yanga ina, ndiyo Chomanganitsa, kuti ndithetse chibale cha pakati pa Yuda ndi Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Kenaka ndidathyolanso ndodo ina ija yotchedwa “Umodzi,” kusonyeza kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Kenaka ndinathyola ndodo yanga yachiwiri yotchedwa Umodzi, kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 11:14
14 Mawu Ofanana  

Ndipo nsanje ya Efuremu idzachoka, ndi iwo amene avuta Yuda adzadulidwa; Efuremu sachitira nsanje Yuda, ndi Yuda sachitira nsanje Efuremu.


Manase adzadya Efuremu; ndi Efuremu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israele; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.


Pakuti sindidzachitiranso chifundo okhala m'dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m'dzanja la mnansi wake, ndi m'dzanja la mfumu yake; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m'dzanja mwao sindidzawalanditsa.


M'mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; ina ndinaitcha Chisomo, inzake ndinaitcha Chomanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.


Pamenepo ndinati, Sindidzadyetsanso inu; chilikufa chife; chosoweka chisoweke; ndi zotsala zidyane, chonse nyama ya chinzake.


Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake.


Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sungathe kukhazikika.


Koma ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungaonongane.


Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.


Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa