Zekariya 11:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo ndinatenga ndodo yanga Chisomo, ndi kuidula pakati, kuti ndiphwanye pangano langa ndinalichita ndi mitundu yonse ya anthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo ndinatenga ndodo yanga Chisomo, ndi kuidula pakati, kuti ndiphwanye pangano langa ndinalichita ndi mitundu yonse ya anthu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Pambuyo pake ndidatenga ndodo yanga ija yotchedwa “Kukoma mtima” ndi kuithyola, kusonyeza kuphwanya chipangano chimene ndidaapangana ndi mitundu yonse ya anthu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Kenaka ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Kukoma mtima ndi kuyithyola, kuphwanya pangano limene ndinachita ndi mitundu yonse ya anthu. Onani mutuwo |
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.