Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 9:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yake, ndi zonse anachita mu Ejipito,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yake, ndi zonse anachita m'Ejipito,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Ife tachoka kutali kwambiri, chifukwa choti tamva za Chauta, Mulungu wanu. Tamva mbiri yonse ya zimene Iye adachita ku Ejipito,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Iwo anayankha kuti, “Akapolo anufe tachokera ku dziko lakutali chifukwa tamva za Yehova Mulungu wanu. Tamva mbiri yonse ya zimene Iye anachita ku Igupto,

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 9:9
21 Mawu Ofanana  

Ndiponso kunena za mlendo, wosati wa anthu anu Aisraele, koma wakufumira m'dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu,


Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.


Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.


Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.


Anachita chodabwitsa pamaso pa makolo ao, m'dziko la Ejipito kuchidikha cha Zowani.


Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.


Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira; kuda mtima kwagwira anthu okhala mu Filistiya.


Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa padziko lonse lapansi.


Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwe, ndi mtundu umene sunakudziwe udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele; pakuti Iye wakukometsa.


Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.


Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepo amitundu amene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti,


Pamenepo Mose anatumiza amithenga ochokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israele, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera;


Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawatulukira, yofuula ndi mau aakulu; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anachiritsidwa.


Ndipo kudzali, ukakubwezerani mau a mtendere, ndi kukutsegulirani, pamenepo anthu onse opezeka m'mwemo akhale akapolo anu, nadzakugwirirani ntchito yathangata.


Muzitero nayo mizinda yonse yokhala kutalitali ndi inu, yosakhala mizinda ya amitundu awa.


ndi zonse anachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basani wokhala ku Asitaroti.


Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao.


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumizinda yao tsiku lachitatu. Koma mizinda yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.


Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa