Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 9:5 - Buku Lopatulika

5 ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, ndipo zinavala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, nizivala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adavala nsapato zothaitha za zigamba zokhazokha, ndiponso zovala zansanza. Buledi amene adatenga anali wouma ndi wachuku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Anthuwa anavala nsapato zakutha ndi zazigamba ndiponso anavala sanza. Buledi wawo yense anali wowuma ndi wowola.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 9:5
7 Mawu Ofanana  

Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake;


Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu; zovala zanu sizinathe pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinathe pa phazi lanu.


Nsapato zako zikhale za chitsulo ndi mkuwa; ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.


Mkate wathu uwu tinadzitengera kamba m'nyumba zathu, ukali wamoto, tsiku lotuluka ife kudza kwanu kuno; koma tsopano, taonani uli wouma ndi woyanga nkhungu;


ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang'ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, chifukwa cha ulendo wochokera kutali ndithu.


zinachita momchenjerera, ndipo zinapita mooneka ngati mithenga, ndipo zinatenga matumba akale pa abulu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong'ambika ndi omangamanga;


Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, ndipo zinati kwa iye ndi kwa amuna a Israele, Tachokera dziko lakutali, chifukwa chake mupangane nafe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa