Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 9:4 - Buku Lopatulika

4 zinachita momchenjerera, ndipo zinapita mooneka ngati mithenga, ndipo zinatenga matumba akale pa abulu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong'ambika ndi omangamanga;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 zinachita momchenjerera, nizimuka nizioneka ngati mithenga, nizitenga matumba akale pa abulu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong'ambika ndi omangamanga;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 adaganiza zoti amugwire m'maso. Adapita nasenzetsa abulu chakudya cha m'matumba akalekale, ndiponso matumba a vinyo a chikopa cha zigamba zokhazokha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 anaganiza zochita zachinyengo. Anapita nasenzetsa abulu awo chakudya mʼmatumba akalekale ndiponso matumba a vinyo achikopa ongʼambikangʼambika.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 9:4
12 Mawu Ofanana  

Ndipo ana ake aamuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao,


Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira; koma sindiiwala malemba anu.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Kapena samathira vinyo watsopano m'matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba aonongeka; koma athira vinyo watsopano m'matumba atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika.


Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano.


Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.


Mkate wathu uwu tinadzitengera kamba m'nyumba zathu, ukali wamoto, tsiku lotuluka ife kudza kwanu kuno; koma tsopano, taonani uli wouma ndi woyanga nkhungu;


ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang'ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, chifukwa cha ulendo wochokera kutali ndithu.


Koma pamene nzika za Gibiyoni zinamva zimene Yoswa adachitira Yeriko ndi Ai,


ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, ndipo zinavala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa