Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 8:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m'molalira, nakhala pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m'molalira, nakhala pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Motero Yoswa adaŵatuma, ndipo iwo adapita ku malo obisalakowo kukaulalira mzindawo. Malowo anali cha kuzambwe kwa Ai, pakati pa Ai ndi Betele. Koma Yoswa ndi gulu lake lankhondo adakhala m'zithando usiku wonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Yoswa atawatumiza, anapita ku malo wokabisalakowo ndipo anadikirira kumeneko. Malowa anali pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai. Koma Yoswa anagona usiku umenewu pakati pa gulu lake lankhondo.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 8:9
9 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.


Momwemo naolotsa mphatso patsogolo pake: ndipo iye yekha anagona usiku womwewo pachigono.


Anthu a ku Betele ndi Ai, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.


Amuna a ku Betele ndi Ai, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu.


Ndipo Yoswa anatuma amuna kuchokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Betaveni, kum'mawa kwa Betele; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.


Ndipo Yoswa analawira m'mamawa, nayesa anthu, nakwera, iye ndi akulu a Israele, pamaso pa anthu a ku Ai.


Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m'molalira pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda.


Ndipo kudzali, mutagwira mzinda, muzitentha mzindawo ndi moto; muzichita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani.


Anatumiza kwa iwo a ku Betele, ndi kwa iwo a ku Ramoti wa kumwera, ndi kwa iwo a ku Yatiri;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa