Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 8:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo kudzali, mutagwira mzinda, muzitentha mzindawo ndi moto; muzichita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo kudzali, mutagwira mudzi, muzitentha mudziwo ndi moto; muzichita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mutaulanda, dzauyatseni moto, monga Chauta walamulira. Ameneŵa ndiwo malamulo amene ndakupatsani.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mukakawulanda mzindawo mudzawuyatse moto. Mukachite monga mwa mawu a Yehova. Amenewa ndiwo malamulo amene ndakupatsani.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 8:8
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu analamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna.


Koma za mizinda ya amitundu awa, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ikhale cholowa chanu, musasiyepo chamoyo chilichonse chakupuma;


Ndipo anamyankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzachita, ndipo kulikonse mutitumako tidzamuka.


Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.


Ndipo anatentha mzinda ndi moto, ndi zonse zinali m'mwemo; koma siliva ndi golide ndi zotengera zamkuwa ndi zachitsulo anaziika m'mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.


Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mzinda, ndi olalira ao kumadzulo kwa mzinda, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa chigwa.


ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng'ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mzinda.


A kumzindanso anawatulukira; potero anakhala pakati pa Israele, ena mbali ina, ena mbali ina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsale kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense.


Ndipo Yoswa anatentha Ai, nausandutsa muunda ku nthawi yonse, bwinja kufikira lero lino.


pamenepo muziuka m'molalira ndi kulowa m'mzinda; pakuti Yehova Mulungu wanu; adzaupereka m'manja mwanu.


Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m'molalira, nakhala pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.


Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke mu Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa