Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 8:16 - Buku Lopatulika

16 Pamenepo anthu onse okhala m'mzinda, anaitanidwa awapirikitse, nampirikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pamenepo anthu onse okhala m'mudzi, anaitanidwa awapirikitse, nampirikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mudzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Anthu onse amumzindamo adauzidwa kuti aŵatsate pambuyo, ndipo pamene ankapirikitsa Yoswa, iyeyo ankathaŵira kutsogolo ndithu, kutalikirana ndi mzinda wao uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Anthu onse a ku Ai anawuzidwa kuti awapirikitse. Ndipo iwo anapirikitsadi Yoswa uja, ndi kupita kutali ndi mzinda wawo.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 8:16
8 Mawu Ofanana  

Anadziwika Yehova, anachita kuweruza, woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake.


Ndipo sanatsale mwamuna mmodzi yense mu Ai kapena mu Betele osatulukira kwa Israele; nasiya mzinda wapululu, napirikitsa Israele.


pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.


Natuluka ana a Benjamini kukomana ndi anthuwo, nakokedwa kutali ndi mzinda, nayamba kuwakantha ndi kuwapha anthu aamuna a Israele, ngati makumi atatu monga nthawi zina, m'makwalala, limodzi la awo lokwera kunka ku Betele, ndi lina ku Gibea kuthengo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa