Yoswa 8:1 - Buku Lopatulika1 Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ake ndi mzinda wake ndi dziko lake; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ake ndi mudzi wake ndi dziko lake; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pambuyo pake Chauta adauza Yoswa kuti, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga ankhondo onse, ndipo upite nawo ku Ai. Ndidzapereka m'manja mwanu mfumu ya ku Ai pamodzi ndi anthu ake onse. Mzindawo pamodzi ndi dzikolo, zonsezo zidzakhala zanu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga gulu lonse la nkhondo, ndipo upite ku Ai. Taona, ndapereka mfumu ya Ai pamodzi ndi anthu ake, mzinda wake ndi dziko lake lonse mʼmanja mwako. Onani mutuwo |
kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.