Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 7:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapirikitsa kuyambira pachipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapirikitsa kuyambira pachipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Anthu a ku Ai adathamangitsa Aisraele kuchokera ku chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya. Aisraele okwanira ngati 36 adaphedwa, makamaka pamene ankatsika phiri. Motero Aisraele onse adataya mtima, ndipo adachita mantha kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Anthu a ku Ai anathamangitsa Aisraeli kuchokera pa chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya ndipo anapha anthu 36. Iwowa anawapha pamene ankatsika phiri. Choncho mitima ya anthu inasweka ndipo analibenso mphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 7:5
10 Mawu Ofanana  

Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.


Apitetu ngati madzi oyenda; popiringidza mivi yake ikhale yodukaduka.


Chifukwa chake manja onse adzafooka, ndi mitima yonse ya anthu idzasungunuka;


Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo chifukwa ninji? Uzikati, Chifukwa cha mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uliwonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uliwonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona ilinkudza, inde idzachitika, ati Ambuye Yehova.


Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.


Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.


Ndipo Aamori, akukhala m'mapiri muja, anatuluka kukomana ndi inu, nakupirikitsani, monga zimachita njuchi, nakukanthani mu Seiri, kufikira ku Horoma.


Ndipo titamva ichi mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m'mwamba umo, ndi padziko lapansi.


nati kwa amunawo, Ndidziwa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, ndi kuti kuopsa kwanu kwatigwera, ndi kuti okhala m'dziko onse asungunuka pamaso panu.


Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa