Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 6:7 - Buku Lopatulika

7 Nati kwa anthu, Pitani, muzizungulira mzinda, ndi ankhondo ndi zida zao atsogolere likasa la Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Nati kwa anthu, Pitani, muzizungulira mudzi, ndi ankhondo ndi zida zao atsogolere likasa la Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndipo adauza anthu kuti, “Yambamponi. Yendani mozungulira mzindawo, ankhondo akhale patsogolo pa Bokosi lachipangano.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndipo analamulira anthu kuti, “Yambani kuyenda! Yendani mozungulira mzinda ndipo ankhondo akhale patsogolo pa Bokosi la Yehova.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 6:7
5 Mawu Ofanana  

Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m'dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordani; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza;


ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.


Ndipo muzizungulira mzinda inu nonse ankhondo, kuuzungulira mzinda kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzani likasa la chipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova.


Ndipo atanena kwa anthu Yoswa, ansembe asanu ndi awiri akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo pamaso pa Yehova, anapita naliza mphalasazo; ndipo likasa la chipangano cha Yehova linawatsata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa