Yoswa 6:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mzindawo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mudziwo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Ansembe asanu ndi aŵiri, aliyense lipenga la nyanga yankhosa lili kumanja, ndiwo azitsogolera Bokosi lachipangano. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, iwe ndi ankhondowo, mudzazungulire mzinda umenewu kasanunkaŵiri, ansembe akuliza malipengawo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Ansembe asanu ndi awiri, atanyamula malipenga a nyanga za nkhosa zazimuna, akhale patsogolo pa Bokosi la Chipangano. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzazungulire mzindawu kasanu ndi kawiri ansembe akuliza malipenga. Onani mutuwo |
Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki Yobu.