Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 6:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo muzizungulira mzinda inu nonse ankhondo, kuuzungulira mzinda kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo muzizungulira mudzi inu nonse ankhondo, kuuzungulira mudzi kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Iwe pamodzi ndi ankhondo, muzizungulira mzinda umenewu masiku asanu ndi limodzi, kamodzi pa tsiku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse muzizungulira mzindawu masiku asanu ndi limodzi, kamodzi pa tsiku.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 6:3
9 Mawu Ofanana  

Ndi pansi pake panali mafaniziro a ng'ombe zakulizinga, khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pake. Ng'ombe zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.


Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.


Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;


Ndipo anazungulitsa likasa la Yehova mzinda, kuzungulira kamodzi; pamenepo analowa kuchigono, nagona m'mwemo.


Ndipo tsiku lachiwiri anazungulira mzinda kamodzi, nabwera kuchigono; anatero masiku asanu ndi limodzi.


Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m'dzanja lako Yeriko ndi mfumu yake, ndi ngwazi zake.


Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mzindawo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo.


Nati kwa anthu, Pitani, muzizungulira mzinda, ndi ankhondo ndi zida zao atsogolere likasa la Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa