Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 6:1 - Buku Lopatulika

1 Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa chifukwa cha ana a Israele, panalibe wotuluka, panalibenso wolowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa chifukwa cha ana a Israele, panalibe wotuluka, panalibenso wolowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mzinda wa Yeriko udaali utatsekedwa pa zipata zake zonse, kuti Aisraele asaloŵe. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotuluka kapena kuloŵa mumzindamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsono mzinda wa Yeriko unali utatsekedwa kuti Aisraeli asalowe. Palibe amene amatuluka kapena kulowa.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 6:1
12 Mawu Ofanana  

Pamene anachiuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anachita manyazi aakulu. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndevu zanu; zitamera mubwere.


Koma mfumu ya Asiriya anampeza Hoseya alikuchita chiwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Ejipito, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asiriya, monga akachita chaka ndi chaka; chifukwa chake mfumu ya Asiriya anamtsekera, nammanga m'kaidi.


Ndipo Eliya anati kwa iye, Elisa, ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yeriko. Nati iye, Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani. Motero anadza ku Yeriko.


Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.


natsika kuchokera ku Yanowa, kunka ku Ataroti, ndi ku Naara, nafika ku Yeriko, natuluka ku Yordani.


Koma mizinda ya fuko la ana a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiyo Yeriko, ndi Betehogila, ndi Emekezizi;


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lake Rahabi, nagona momwemo.


Ndipo anati kwa Yoswa, Zoonadi, Yehova wapereka dziko lonse m'manja mwathu; ndiponso nzika zonse zasungunuka pamaso pathu.


Ndipo amunawo anawalondola panjira ya ku Yordani yonka kudooko; ndipo atatuluka akuwalondola, anatseka pachipata.


Ndipo kazembe wa ankhondo a Yehova anati kwa Yoswa, Vula nsapato yako pa phazi lako; pakuti malo upondapo mpopatulika. Nachita Yoswa chomwecho.


Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m'dzanja lako Yeriko ndi mfumu yake, ndi ngwazi zake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa