Yoswa 5:7 - Buku Lopatulika7 Koma ana ao aamuna amene anawautsa m'malo mwao, iwowa Yoswa anawadula; popeza anakhala osadulidwa, pakuti sanawadule panjira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Koma ana ao amuna amene anawautsa m'malo mwao, iwowa Yoswa anawadula; popeza anakhala osadulidwa, pakuti sanawadule panjira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Koma ana ao amene adaloŵa m'malo mwao, sadaumbalidwe pamene anali paulendo m'chipululumo, ndipo ndiwo amene Yoswa adalamula kuti aumbalidwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Koma ana awo amene analowa mʼmalo mwawo ndiwo amene Yoswa anawachita mdulidwe popeza sanachite pamene anali pa ulendo wawo mʼchipululu muja. Onani mutuwo |
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.