Yoswa 5:6 - Buku Lopatulika6 Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka m'Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Aisraele adakhala akuyenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka adafa amuna onse amene potuluka ku Ejipito anali a msinkhu woyenera pa nkhondo. Adatha nkufa, popeza kuti sadamvere Chauta. Iye adaachita kuŵalumbirira kuti sadzaloŵamo m'dziko lamwanaalirenji lija limene adaalonjeza kwa makolo ao kuti adzaŵapatsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Aisraeli anakhala akuyenda mʼchipululu kwa zaka makumi anayi mpaka amuna onse amene potuluka mʼdziko la Igupto anali a msinkhu woyenera kupita ku nkhondo anamwalira. Iwo anafa chifukwa sanamvere mawu a Yehova. Yehova anawalumbirira kuti sadzalowa konse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi limene analonjeza kwa makolo awo kuti adzatipatsa. Onani mutuwo |