Yoswa 5:5 - Buku Lopatulika5 Pakuti anthu onse anatulukawo anadulidwa; koma anthu onse obadwa m'chipululu panjira potuluka mu Ejipito sanadulidwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Pakuti anthu onse anatulukawo anadulidwa; koma anthu onse obadwa m'chipululu panjira potuluka m'Ejipito sanadulidwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Anthu onse amene adaatuluka ku Ejipito anali ataumbalidwa kale, koma onse obadwira m'chipululu pa nthaŵi ya ulendo wofuma ku Ejipito anali osaumbalidwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Anthu onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto anali atachita mwambo wa mdulidwe, koma onse amene anabadwira mʼchipululu, pa ulendo wochoka ku Igupto, sanachite. Onani mutuwo |
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.