Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 5:4 - Buku Lopatulika

4 Koma chifukwa chakuti Yoswa anawadula ndi ichi: anthu onse otuluka mu Ejipito, anthu aamuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'chipululu panjira, atatuluka mu Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma chifukwa chakuti Yoswa anawadula ndi ichi: anthu onse otuluka m'Ejipito, anthu amuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'chipululu panjira, atatuluka m'Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Adachita zimenezi chifukwa amuna amene anali oyenera kuponya nkhondo onse adaatha nkufa m'chipululu atatuluka ku Ejipito kuja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Chifukwa chimene Yoswa anachitira izi ndi ichi: Onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto, amuna onse amene anali oyenera kumenya nkhondo anatha kufa mʼchipululu atatuluka mʼdziko la Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 5:4
8 Mawu Ofanana  

popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;


Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwere nao; pakuti anamwazika m'chipululu.


Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira.


Ndipo kunali, atatha kufa amuna onse ankhondo mwa anthu,


Ndipo Yoswa anadzisemera mipeni yamiyala nadula ana a Israele pa Gibea-Naraloti.


Pakuti anthu onse anatulukawo anadulidwa; koma anthu onse obadwa m'chipululu panjira potuluka mu Ejipito sanadulidwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa