Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 4:5 - Buku Lopatulika

5 nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordani, nimudzisenzere yense mwala paphewa pake, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordani, nimudzisenzere yense mwala paphewa pake, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 ndipo adaŵalamula kuti, “Loŵani mu mtsinje wa Yordaniwu patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wanu. Aliyense mwa inu atenge mwala pa phewa. Fuko lililonse la Aisraele litenge mwala umodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 ndipo anawawuza kuti, “Lowani pakati pa mtsinje wa Yorodani, patsogolo pa Bokosi la Yehova Mulungu wanu. Ndipo aliyense wa inu atenge mwala pa phewa lake, monga mwa chiwerengero cha mafuko a Aisraeli,

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 4:5
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anati kwa abale ake, Sonkhanitsani miyala; ndipo anasonkhanitsa miyala nakundika mulu: ndipo anadya pamulupo.


Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Ndipo kudzali, tsiku lakuoloka inu Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, kuti mudziutsire miyala yaikulu, ndi kuimata ndi njeresa;


Imvani Israele; mulikuoloka Yordani lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akulu ndi amphamvu akuposa inu, mizinda yaikulu ndi ya malinga ofikira kuthambo,


Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordani, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anamanga ku Yordani guwa la nsembe, guwa lalikulu maonekedwe ake.


Pamenepo Yoswa anaitana amuna khumi ndi awiriwo amene anawaikiratu mwa ana a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi;


kuti ichi chikhale chizindikiro pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani ndi inu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa