Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 4:3 - Buku Lopatulika

3 ndipo muwalamulire iwo ndi kuti, Mudzitengere pano pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe, miyala khumi ndi iwiri, ndi kuoloka nayo, ndi kuiika m'mogona m'mene mugonamo usiku uno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 ndipo muwalamulire iwo ndi kuti, Mudzitengere pano pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe, miyala khumi ndi iwiri, ndi kuoloka nayo, ndi kuiika m'mogona m'mene mugonamo usiku uno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono uŵalamule kuti, ‘Tengani miyala khumi ndi iŵiri pakati penipeni pa mtsinje wa Yordanipo, pa malo amene anali kuimirira ansembewo. Nyamulani miyala imeneyo ndi kudza nayo ku zithando zanu kumene mudzagone usiku.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsono uwalamule kuti, ‘Tengani miyala khumi ndi iwiri pakati penipeni pa mtsinje wa Yorodani, pamalo pamene ansembe anayimirirapo. Miyalayo muwoloke nayo ndi kudzayitula pamalo pamene mukagone usiku uno.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 4:3
11 Mawu Ofanana  

ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.


Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:


Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.


Ndipo anayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa khala chete miyala idzafuula.


Ndipo Yoswa anati kwa anthu onse, Taonani, mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa; pakuti udamva mau onse a Yehova amene ananena kwa ife; ndipo udzakhala mboni yotsutsa inu, mungakanize Mulungu wanu.


Ndipo kudzakhala, akaima mapazi a ansembe akusenza likasa la Yehova Ambuye wa dziko lonse, m'madzi a Yordani, adzadulidwa madziwo, ndiwo madzi ochokera kumagwero, nadzaima mulu umodzi.


Pamenepo Yoswa anaitana amuna khumi ndi awiriwo amene anawaikiratu mwa ana a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi;


Ndipo ana a Israele anachita monga Yoswa anawalamulira, nasenza miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, monga Yehova adalankhula ndi Yoswa, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele; ndipo anaoloka nayo kunka kogona, naiika komweko.


Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa