Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 4:13 - Buku Lopatulika

13 ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Asilikali ngati zikwi makumi anai adaoloka, nakaima pa tsidya, m'chigwa cha Yeriko, ali okonzekera nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Asilikali pafupifupi 40,000 anawoloka napita kukayima mʼchigwa cha Yeriko kukonzekera nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 4:13
11 Mawu Ofanana  

Koma nkhondo ya Ababiloni inalondola mfumu, nayipeza m'zidikha za Yeriko; koma nkhondo yake yonse inambalalikira.


Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israele anakwera kuchokera m'dziko la Ejipito okonzeka.


Koma nkhondo ya Ababiloni inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu.


Koma nkhondo ya Ababiloni inamtsata mfumu, nimpeza Zedekiya m'zidikha za ku Yeriko; ndipo nkhondo yake yonse inambalalikira iye.


koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang'ono athu adzakhala mizinda ya malinga chifukwa cha okhala m'dzikomo.


Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.


Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele.


Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;


Tsiku lomwelo Yehova anakulitsa Yoswa pamaso pa Aisraele onse; ndipo anamuopa monga anaopa Mose, masiku onse a moyo wake.


Ndipo ana a Israele anamanga misasa ku Giligala; nachita Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, madzulo, m'zidikha za Yeriko.


Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa