Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 4:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ansembe atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta adatsogolera anthu onse aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Anthu atatha kuwoloka, ansembe anatsogolera anthuwo atanyamula Bokosi la Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 4:11
7 Mawu Ofanana  

Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu.


Pamenepo munaoloka Yordani, ndi kufika ku Yeriko; ndi eni ake a ku Yeriko anaponyana nanu nkhondo, Aamori, ndi Aperizi, ndi Akanani, ndi Ahiti, ndi Agirigasi, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu.


Ndipo ansembe akulisenza likasa la chipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordani, ndi Aisraele onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordani.


Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la chipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordani muziima mu Yordani.


Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordani, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.


Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;


Ndipo kunali, atakwera ansembe akusenza likasa la chipangano la Yehova, kutuluka pakati pa Yordani, nakwera pamtunda mapazi a ansembe, madzi a mu Yordani anabwera m'njira mwake, nasefuka m'magombe ake onse monga kale.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa