Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 3:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la chipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordani muziima mu Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la chipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordani muziima m'Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ansembe amene akunyamula Bokosi lachipangano la Chauta, uŵalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yordani, muloŵe m'madzimo ndi kuima m'mphepete.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ansembe amene akunyamula Bokosi la Chipangano uwalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yorodani mulowe mu mtsinjemo ndi kuyima mʼmphepete.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 3:8
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordani. Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.


Ndipo anamemeza abale ao, nadzipatula, nalowa monga adawauza mfumu mwa mau a Yehova, kuyeretsa nyumba ya Yehova.


Nanena Hezekiya kuti apereke nsembe yopsereza paguwa la nsembe. Ndipo pakuyamba nsembe yopsereza, inayambanso nyimbo ya Yehova ndi malipenga, pamodzi ndi zoimbira za Davideyo mfumu ya Israele.


Hezekiya mfumu ndi akalonga nauzanso Alevi aimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anaimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira.


Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kuchita chowauza mfumu ndi akulu mwa mau a Yehova.


Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.


Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse.


Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.


Ndipo ansembe akulisenza likasa la chipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordani, ndi Aisraele onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordani.


nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo muchoke kwanu ndi kulitsata.


Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisraele onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.


Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israele, Idzani kuno, mumve mau a Yehova Mulungu wanu.


Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa