Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 3:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la chipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la chipangano, natsogolera anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la chipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la chipangano, natsogolera anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 M'maŵa mwake Yoswa adauza ansembe kuti, “Nyamulani Bokosi lachipangano la Chauta, muwoloke, mutsogolere anthuwo.” Iwowo adachitadi monga momwe Yoswa adanenera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mmawa mwake Yoswa ananena kwa ansembe kuti, “Nyamulani Bokosi la Chipangano muwoloke ndipo mukhale patsogolo pa anthu.” Motero iwo analinyamula ndi kupita patsogolo pawo.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 3:6
11 Mawu Ofanana  

Ndipo akulu onse a Israele anadza, ansembe nanyamula likasa.


Nadza akuluakulu onse a Israele, nanyamula likasalo Alevi.


Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.


Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.


Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepo amitundu amene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti,


m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo muchoke kwanu ndi kulitsata.


Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati pa inu.


Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisraele onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzani likasa la chipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa