Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 3:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kuchoka ku Sitimu, nafika ku Yordani, iye ndi ana onse a Israele; nagona komweko, asanaoloke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kuchoka ku Sitimu, nafika ku Yordani, iye ndi ana onse a Israele; nagona komweko, asanaoloke.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 M'mamaŵa kutacha Yoswa adanyamuka. Iye, pamodzi ndi Aisraele onse, adatuluka ku Sitimu kuja, napita ku Yordani, ndipo adagona kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yoswa ndi Aisraeli onse anadzuka mmamawa nanyamuka ku Sitimu kupita ku Yorodani. Iwo anagona kumeneko asanawoloke mtsinje wa Yorodaniwo.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 3:1
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.


Ndinafulumira, osachedwa, kusamalira malamulo anu.


Kuyambira chaka chakhumi ndi chitatu cha Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero lomwe, zakazi makumi awiri ndi zitatu, mau a Yehova anafika kwa ine, ndipo ndanena kwa inu, pouka mamawa ndi kunena; koma simunamvere.


kumvera mau a atumiki anga aneneri, amene ndituma kwa inu, pouka mamawa ndi kuwatuma iwo, koma simunamvere;


Ndipo tsopano, chifukwa munachita ntchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamve; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankhe;


Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.


Ndipo Israele anakhala mu Sitimu, ndipo anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana aakazi a Mowabu;


Ndipo m'mawa mwake anauka usikusiku, natuluka namuka kuchipululu, napemphera kumeneko.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lake Rahabi, nagona momwemo.


Ndipo Yoswa analawira mamawa, ndi ansembe anasenza likasa la Yehova.


Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri analawira mamawa, mbandakucha, nazungulira mzinda mommuja kasanu ndi kawiri; koma tsiku lijalo anazungulira mzinda kasanu ndi kawiri.


Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayandikizitsa Israele, fuko ndi fuko; ndi fuko la Yuda linagwidwa;


Ndipo Yoswa analawira m'mamawa, nayesa anthu, nakwera, iye ndi akulu a Israele, pamaso pa anthu a ku Ai.


Nauka ana a Israele m'mawa, naumangira Gibea misasa.


Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Yese; ndipo iye anafika ku linga la magaleta, napeza khamu lilikutuluka kunka poponyanira nkhondo lilikufuula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa