Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 24:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israele ku Sekemu, naitana akuluakulu a Israele ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao; ndipo anadzionetsa pamaso pa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israele ku Sekemu, naitana akuluakulu a Israele ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao; ndipo anadzilangiza pamaso pa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsono Yoswa adasonkhanitsa mafuko onse a Aisraele ku Sekemu. Adaitana akuluakulu, atsogoleri, aweruzi ndi akapitao a Aisraele, ndipo onsewo adafika pamaso pa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsono Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israeli ku Sekemu. Iye anayitanitsa akuluakulu, atsogoleri, oweruza, ndi akuluakulu a boma la Israeli, ndipo iwo anafika pamaso pa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 24:1
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anapitirira m'dzikomo kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.


Ndipo anampatsa Yakobo milungu yachilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu.


Ndipo Rehobowamu ananka ku Sekemu, popeza Aisraele onse anadza ku Sekemu kumlonga ufumu.


Pamenepo mfumu inatumiza anthu, namsonkhanitsira akulu onse a Yuda ndi a mu Yerusalemu.


Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.


Chifukwa chake sungani mau a chipangano ichi ndi kuwachita, kuti muchite mwanzeru m'zonse muzichita.


Ndipo anapatula Kedesi mu Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.


Yoswa anaitana Aisraele onse, akuluakulu ao, ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri;


Pamenepo ana onse a Israele ndi anthu onse anakwera nafika ku Betele, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.


koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Chifukwa chake tsono mudzionetse pamaso pa Yehova mafukomafuko, ndi magulumagulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa