Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 23:3 - Buku Lopatulika

3 ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anachitira mitundu iyi yonse ya anthu chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anachitira mitundu iyi yonse ya anthu chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Zonse zimene Chauta wachitira mitundu ina yonseyi chifukwa cha inu, mwazipenya. Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene wakumenyerani nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Inu mwaona zonse zimene Yehova Mulungu wanu wachita kwa mitundu yonseyi chifukwa cha inu. Ndi Yehova Mulungu wanu amene anakumenyerani nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 23:3
13 Mawu Ofanana  

Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.


Inu munaona chimene ndinachitira Aejipito; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha.


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkulu kupitirira malire a Israele.


Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, Iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu;


pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani.


Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.


Mukadzanena m'mtima mwanu, Amitundu awa andichulukira; ndikhoza bwanji kuwapirikitsa?


Adzaperekanso mafumu ao m'dzanja mwanu, ndipo muwafafanize maina ao pansi pa thambo; palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga.


Ndipo panalibe tsiku lotere kale lonse kapena m'tsogolomo, lakuti Yehova anamvera mau a munthu; pakuti Yehova anathirira Israele nkhondo.


Ndipo Yoswa anagwira mafumu awa onse ndi dziko lao nthawi yomweyi; chifukwa Yehova Mulungu wa Israele anathirira Israele nkhondo.


Munthu mmodzi wa inu adzapirikitsa anthu chikwi chimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa