Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 23:2 - Buku Lopatulika

2 Yoswa anaitana Aisraele onse, akuluakulu ao, ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yoswa anaitana Aisraele onse, akuluakulu ao, ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono Yoswayo adaitana Aisraele onse, pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, aweruzi ndi akapitao a anthuwo, naŵauza kuti “Tsopano ine ndakalamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yoswayo anayitanitsa Aisraeli onse pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, oweruza, ndi oyangʼanira anthu antchito ndipo anawawuza kuti, “Ine ndakalamba ndipo ndili ndi zaka zambiri.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 23:2
11 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu Davide anakalamba nachuluka masiku ake; ndipo iwo anamfunda ndi zofunda, koma iye sanafundidwe.


Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni mu Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova m'mzinda wa Davide, ndiwo Ziyoni.


Ndipo anasonkhanitsa akulu onse a Israele, ndi ansembe ndi Alevi.


ndi woyang'anira minda yampesa ndiye Simei Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yampesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifamu;


Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.


Ndisonkhanitsire akulu onse a mafuko anu, ndi akapitao anu, kuti ndinene mau awa m'makutu mwao, ndi kuchititsa mboni kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse iwo.


Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikulukulu, alilandire cholowa chao.


ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anachitira mitundu iyi yonse ya anthu chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.


Ndipo Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israele ku Sekemu, naitana akuluakulu a Israele ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao; ndipo anadzionetsa pamaso pa Mulungu.


Ndipo tsopano, siyi mfumu idzayendabe pamaso panu; ndipo ine ndine wokalamba waimvi; ndipo, onani, ana anga aamuna ali nanu, ndipo ine ndinayendabe pamaso panu kuyambira ubwana wanga kufikira lero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa