Yoswa 22:11 - Buku Lopatulika11 Ndipo ana a Israele anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anamanga guwa la nsembe pandunji padziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordani, ku mbali ya ana a Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo ana a Israele anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anamanga guwa la nsembe pandunji pa dziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordani, ku mbali ya ana a Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Tsono Aisraele ena onse adauzidwa kuti, “Tamvani! Anthu onse a fuko la Rubeni ndi la Gadi, pamodzi ndi theka lija la fuko la Manase adamanga guwa ku Geliloti m'malire a dziko la Kanani, tsidya lakuno la Yordani, moyang'anana ndi Israele.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Ndipo pamene Aisraeli ena onse anawuzidwa kuti anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase amanga guwa lansembe mʼmalire a Kanaani ku Geliloti, ku tsidya lathu lino la Yorodani, Onani mutuwo |
Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m'dziko la cholowa cha Yehova m'mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.