Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 21:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo maere anatulukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa fuko la Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la Benjamini, mizinda khumi ndi itatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo maere anatulukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa fuko la Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la Benjamini, midzi khumi ndi itatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mabanja a Kohati ndiwo anali oyambirira kupatsidwa mizinda. Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aroni adapatsidwa mizinda 13, kuchokera m'mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Maere oyamba anagwera mabanja a Kohati, Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aaroni anapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 21:4
9 Mawu Ofanana  

Ndi mbale wake Asafu wokhala ku dzanja lake lamanja, ndiye Asafu mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,


Ndipo maina a ana aamuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.


Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.


Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.


Ndipo ana a Israele anapatsa Alevi, kutapa pa cholowa chao, monga mwa lamulo la Yehova, mizinda iyi ndi mabusa ao.


Ndipo ana otsala a Kohati analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Efuremu, ndi pa fuko la Dani, ndi pa hafu la fuko la Manase, mizinda khumi.


Eleazaranso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika paphiri la Finehasi mwana wake, limene adampatsa ku mapiri a Efuremu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa