Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 21:1 - Buku Lopatulika

1 Pamenepo akulu a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazara wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamenepo akulu a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazara wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsiku lina atsogoleri a mabanja a fuko la Levi adabwera kwa wansembe Eleazara, kwa Yoswa, mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsono atsogoleri a mabanja a fuko la Levi anabwera kwa wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraeli,

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 21:1
9 Mawu Ofanana  

Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa mu Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo mu Israele.


Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana aamuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amenewo ndiwo mabanja a Rubeni.


Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Mowabu, pa Yordani, ku Yeriko, ndi kuti,


Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.


Ndipo awa ndi maiko ana a Israele anawalanda m'dziko la Kanani, amene Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, anawagawira.


Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse cholowa pakati pa abale athu; chifukwa chake anawapatsa monga mwa lamulo la Yehova, cholowa pakati pa abale a atate wao.


Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, zikhale zaozao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la chihema chokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa